M’busa wa mpingo wa Lilongwe CCAP, umene uli pansi pa Synod ya Livingstonia, a Nase Chunga, alangiza anthu amene ali paubwenzi ngakhalenso pabanja kuti ngati akukumana ndi nkhanza zosiyanasiyana, kuphatikizapo kumenyedwa, ndibwino kupulumutsa miyoyo yawo posiyana naye wachikondi oteroyo.
Iwo ati nkhanza zambiri zimachitika kaamba kakuti anthu ambiri sadziwa zoona zenizeni zokhudza chikondi.
Abusa a Chunga atinso chiwelengero cha achinyamata amene akuthetsa mabanja chikukula m’dziko muno popeza mipingo siikutenga nthawi kuphunzitsa achinyamata nkhani zokhudza chikondi komanso makhalidwe a m’banja.
A Chunga anena izi pamene anali ndi tsiku lophunzitsa achinyamata zokhudza mavuto amene amadza kaamba kogwa mchikondi usanakonzeke komanso kukana chikondi kaamba kokhala ndi zokhumba zoposa msinkhu wako.
A Chunga atinso achinyamata ambiri akumangothamangira kulowa m’banja asanadziwane bwinobwino ati poti maubwenzi awo akumakhala odalira lamya komanso kulumikizana pa masamba a mchezo.
Iwo atinso ndipovuta kuti munthu adziwe khalidwe lenileni la wachikondi yemwe ali kutali, kotero ambiri amakadzidzimuka atalowa kale m’banja kuti agwira chikolopa.