Ophunzira pa sukulu yaukachenjede ya University of Malawi(Unima) ku Zomba akhazikitsa chipangizo chothandiza anthu omwe ali ndi ulumali wosaona.
Mmodzi mwa ophunzirawo, Hudson Mwangalika, wati mwa zina, chipangizocho, chomwe amavala ku maso ngati magalasi, chimatulutsa phokoso yemwe wachivalayo akayandikira chinthu kutsogolo kwake. Izi zimathandiza kuti munthuyo asaombane ndi chinthucho.
Izi zadziwika pomwe ophunzirawo amakhazikitsa kampani yawo ya luso lamakono yotchedwa HB Space TL.
Pamwambowo, ophunzirawo anawonetsanso chipangizo chotayiramo zinyalala chotchedwa smart bin chomwe chimatseguka chokha mkati mwake munthu akachiyandikira komanso kuchibaibitsa. Ophunzirawo anawonetsanso zipangizo zina za luso lamakono.
Ndipo m’mau ake, mkulu oona za luso la makono mu unduna wa za maphunziro, Chomora Mikeka, wati zomwe achinyamatawa akonza, zingathandize kuchepetsa ndalama zomwe dziko lino limaononga pogula zipangizo ngati zomwezi kuchokera ku maiko akunja.