Ophunzira ena amene akulemba mayeso a Form Four ku Mangochi achedwa kulemba mayeso awo mmawa walero kaamba kakuti mapepala a mayeso amene amafuna kulemba sanafike.
Malinga ndi mmodzi mwa aphunzitsi amene akuyang’anira nawo mayesowa ku Mangochi, ophunzirawa akuwasunga mzipinda zolembelamo mayeso pamene akuluakulu a ofesi ya zamaphunziro ali mkati mwa ntchito yoonetsetsa kuti mapepala a mayesowa afike.
Ena mwa malo olembetsera mayeso amene akhudzidwa ndi Mangochi Secondary komanso sukulu yasekondale yoyendera ya Mpondasi.
Mneneri wa bungwe la Maneb, Angela Kashitigu, wati mapepala olembera mayesowa anasochera potumizidwa m’boma la Chikwawa mmalo mwa Mangochi.
Pakadali pano, bungweli akuti likukonza za vutoli.
Ophunzirawa akuyembekezeka kulemba phunziro la Physics.
Wolemba: Owen Mavula