Gawo loyamba la ufa umene boma lagula wa ndalama zokwana $20 million othandiza anthu amene akhudzidwa ndi njala tsopano wayamba kufika m’dziko muno.
Boma lagula ufawu kudzera ku bungwe la WFP kuchokera m’maiko a South Africa ndi Tanzania.
Mwambo opereka ufawu ku boma wachitika ku Limbe mu mzinda wa Blantyre.
Mlembi wamkulu mu unduna wa zamalimidwe owona za ulimi wanthilira, a Geoffrey Mamba, ndiwo alandira ufawu ku Limbe kuchokera kwa mkulu wa WFP m’dziko muno, a Paul Turnbull.
Anthu okwana 4.4 million ndiwo akuvutika ndi njala ndipo ufawu onse ukwana ma tani 23,000 ndipo ufikira anthu otere kuyambira mawa loweruka, malinga ndi a Mamba.