Mtsogoleri wa dziko wa lino, Dr Lazarus Chakwera, wati ndiokondwa kuti ntchito zachitukuko zikuyenda m’zigawo zonse komanso aMalawi akuyikapo chidwi, zimene zikusonyeza kuti dziko ndi la aliyense.
Iye adatsindika kuti chitukuko sichiyenera kukhazikika m’dera limodzi lokha.
Polankhula ku Zomba, mtsogoleri wa dziko linoyu wati mnzinda wa Zomba uli ndi mbiri yopatsa chidwi, maka pa nkhani yazomangamanga zokhazikika, monga nyumba zomwe boma la Japan.
Pulezidenti Chakwera watsindikanso zakufunika kopereka mwayi wa ntchito kwa ophunzira amene adamaliza maphunziro awo kusukulu monga ya Domasi, ponena kuti sikwabwino kuti akhale pa ulova.
Ndipo Dr Chakwera alengeza kuti ayitanidwa ku Germany kumene, mwazina, akakambirana ndi mtsogoleri kumeneko zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo za mayendedwe a sitima pa Nyanja ya Malawi.
Olemba: Mercy Zamawa