Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Chitukuko chifalikira m’boma lonse la Nsanje — Zikhale

Nduna ya za m’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma, yalonjeza anthu ku Nsanje kuti boma lipitilira kukhazikitsa ntchito za chitukuko m’bomali ndi cholinga chotukula bizinesi zawo.

Poyankhula pa msonkhano wa chitukuko pa bwalo la Mpatsa CDSS mdera la pakati m’boma la Nsanje, a Zikhale Ng’oma, omwenso ndi mkulu okonza mapulani m’chipani cha MCP, ati ichi ndi chifukwa boma layika chidwi pobwezeretsa maulendo a njanji olumikiza bomali ndi maboma ena komanso dziko la Mozambique.

Pamsonkhanowo, a Ng’oma alandira anthu 300 ochoka ku chipani chotsutsa cha DPP kulowa MCP.

Related posts

KAMPANI ZACHITA BWINO CHAKA CHATHA— MCCCI

Romeo Umali

Aloza chala maboma akale posalabadira nsewu wa Karonga-Chiweta

Romeo Umali

Namondwe Chido wakula mphamvu

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.