Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

“Ntchito zomangamanga zidzikhala zapamwamba”

Prezidenti wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati ndikofunika kuti makontalakitala adzigwira ntchito zapamwamba ndi zolimba.

Pa chifukwachi, Dr Chakwera walamula mlembi mu ofesi ya Prezidenti ndi nduna zake kuti aonetsetse kuti akulondoloza za nkhaniyi.

Mwazina, Dr Chakwera wati ndi wokondwa kuona kuti koleji za
aphunzitsi za Chikwawa, Rumphi komanso Mchinji TTC azimanga mwapamwamba.

Prezidenti Chakwera walankhula zimenezi pamene amatsekulira makoleji a aphunzitsi atatuwa pamwambo omwe unachitikira ku Rumphi mchigawo chakumpoto.

Mtsogoleri wa dziko linoyu ali m’chigawo chakumpoto kuyendera zitukuko zosiyanasiyana komwe watsimikiza kuti boma lake limalizitsa komanso kuyamba zitukuko zomwe anati ndi zokomera a Malawi.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

A budget of hope and optimism

Justin Mkweu

NGOKWE COMMUNITY TAKES LEGISLATOR TO TASK

MBC Online

GERMANY HANDS OVER UNLOCKING TALENT PROJECT TO GVT

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.