Apolisi m’boma la Balaka adandaula ndi kukwera kwa chiwerengero cha milandu yokhuza nkhanza m’mawanja m’bomalo.
Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo, a Gladson M’bumpha, kuchokera mwezi wa January kufika mwezi wa June chaka chino m’bomalo alandira milandu yoposa 280 poyerekeza ndi milandu 180 mu nthawi ngati yomweyi chaka chatha.
Pakadali pano mlembi wamkulu wa bungwe lachipemebezo la Malawi Council of Churches (MCC), m’busa Alemekezeke Phiri wati mipingo mdziko muno ili ndikuthekera kothandiza kuchepetsa nkhanza m’banja.
Mwa zina m’busa Phiri wati nchifukwa chake bungwe la MCC lakhala likuchititsa maphunziro m’maboma ena m’dziko muno kuphatikizapo la Balaka komwe akuphunzitsa atsogoleri a mipingo kuti mu ulaliki wawo adzikambamonso nkhani zokhudza kuipa kwa nkhanza mmabanja.
Olemba: Alufeyo Liyaya