Unduna owona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo wati ndiokhumudwa ndimomwe anthu akupitilizira kuononga nkhalango m’dziko muno.
Mmodzi wa akuluakulu ku undunawu, a Titus Zulu, ndiwo ayankhula izi ku Lusangazi m’chigawo chakumpoto pamene amapereka zipangizo zotetezera nkhalango kwa anthu amene amakhala m’midzi yozungulira nkhalango ya Viphya.
A Zulu ati ndizomvetsa chisoni kuti nkhalango zikupitilira kutha, zomwe zikuonjezera mavuto a kusintha kwanyengo m’dziko muno.
“Kuononga nkhalango ndikudzipweteka tokha chifukwa munkhalangoyi mumapezeka zinthu zambiri zotithandiza ife tomwe ngati anthu,” anatero a Zulu.
Iwo anati kuononga nkhalango kukupangitsa kuti mvula isamabwere mokhulupirika komanso kuti mitsinje idziphwa, zomwe anati zikusokoneza chikonzero cholimbikitsa ulimi wamthilira.
A Zulu anati poona kuti antchito oteteza nkhalango akuchepa, unduna wawo waganiza zogwilira ntchito yoteteza nkhalangozi ndi anthu okhala mozungulira nkhalangozi.
Wolemba: Henry Haukeya