Bungwe la ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya MUBAS la Students Representative Council lati likhala likulangiza ophunzira pasukuluyi pa kagwiritsidwe ntchito kabwino kandalama zomwe amapatsidwa zowathandizira pa moyo wawo wamaphunziro.
Izi zanenedwa potsatira kuwonjezeredwa kwa ndalamazi kuchokera pa K350,000 kufika pa K560,000 pa chaka.
Malinga ndi mtsogoleri wa bungweli, Gershom Nyirenda, wophunzira aliyense ayenera kuwonetsetsa kuti ndalamazi zikugwiritsidwa ntchito pogulira zofunikira za moyo wawo wa tsiku ndi tsiku monga momwe ziyenera kukhalira.
Polankhula mu programme ya The Pot kuno ku MBC, Nyirenda, yemwenso ndi mkulu wa mabungwe a ophunzira msukulu zonse zaukachenjede m’dziko muno, wati sikoyenera kuti ophunzirawa akhale akuchita zinthu zina zosayenera monga kumwa mowa mwauchidakwa pogwiritsa ntchito ndalamazi.
Kuwonjezeredwa kwa ndalamazi kwadza potsatira zomwe adalamula mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, kuti ndalamazi zikwezedwe pofuna kuchepetsa mavuto omwe ophunzirawa akhala akukumana nawo.