Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ophunzira apindilana ndebvu mkamwa

Mpikisano wa masewero a mpira wamanja komanso miyendo wa ophunzira msukulu za ku Machinjiri wa South Lunzu Primary Schools Trophy, wayamba ndi ntibu wa zigoli mbali zonse zampikisanowu.

Pa tsiku loyamba, pa mpira wa atsikana wamanja, Namilango Primary yagonjetsa Mpata School ndi zigoli 5 kwa duu, Nthawira Primary yagonjetsa Makalanga Primary ndi zigoli 15 kwa 6 pomwe Nkolokoti Primary yawonetsa zakuda South Lunzu Primary pomwetsa zigoli 19 kwa 12.

Pa mpira wa miyendo, Nthawira Primary yapambana ndi chigoli chimodzi kwa duu ndi timu ya Makalanga, pomwe South Lunzu yagonjetsa Nkolokoti Primary ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.

Pa masewero ena omwe achitikanso lero mu mpikisano omwewu, Nanjiriri Primary yalempherana ndi SOS pogoletsana chigoli chimodzi kwa chimodzi pomwe Namilango Primary yagonjetsa Mpata School ndi zigoli 5 kwa duu.

Polankhula pokhazikitsa mpikisanowu, yemwe akuthandiza mpikisanowu, a Alex Chimwala, yemwe amachita ntchito zamalonda, anati cholinga chake ndi kutukula masewero m’dziko muno kuyambira kwa achisodzera mmakwalala komanso kuti achinyamata adzilimbikira maphunziro.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Police, Mzuzu residents strengthen ties through community hike

MBC Online

Pamodzi Kuthetsa Nkhanza Project launched

MBC Online

Malawi, Tanzania to implement Songwe River Development Programme

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.