Unduna oona za malonda walangiza onse amene amapanga katundu osiyanasiyana kuti adzipanga katundu wabwino amene angachite bwino pamisika wa mayiko akunja.
Mkulu wazamalonda ku undunawu, a Clement Phangaphanga, anati a malonda asamangoganiza zakatundu ogulitsa m’dziko mokha muno koma adziganiza misika ya kunja ndi cholinga cha kuti m’dziko muno mudzibwera ndalama zakunja zambiri.
A Phangaphanga anayamikira kampani za m’chigawo cha kumpoto zimene zimalandira ziphaso zakatundu zosonyeza kuti wakwanitsa muyeso oyenera wa bungwe la Malawi Bureau of Standards.
“Katundu opangidwa kuno ku Malawi ali ndi kuthekera kokhazikika m’misika yakumayiko akunja monga oyandikana nawo ngati Tanzania, Zambia ngakhale Zimbabwe. Chongofunika ndi luso kuti katunduyu adzikhala wapamwamba,” anatero a Phangaphanga.
Malinga ndi bungwe la Malawi Bureau of Standards, kampani zambiri za m’chigawo cha kumpoto ndizimene zalandira ziphaso zakatundu wawo poyerekeza ndi zigawo zina.
Olemba: Henry Haukeya