Mtsogoleri wa bungwe loyang’anira masewero a mpira wa miyendo padziko lonse la pansi la FIFA, a Gianni Infantino, akuyembekezeka kupepesa mwapadera ku banja la malemu Dr Saulos Chilima amene anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.
Iwo akapepesanso kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera.
A Infantino afika m’dziko muno lachiwiri madzulo kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe pamene analandiridwa ndi mtsogoleri oyendetsa masewero a mpira wa miyendo m’dziko muno, a Fleetwood Haiya.
Koma a Infantino ayimitsa kaye dongosolo limene anakonza kuti ayambepo ntchito yoyendera masewero a mpira wa miyendo kaamba ka chisoni chomwe chakuta dziko la Malawi.