Banki yayikulu padziko lonse ya World Bank yati ndondomeko yazachuma ya dziko la Malawi yachaka cha 2024/2025 yomwe yaperekedwa sabata yatha, ikupereka chiyembekezo kuti chuma chadziko lino chibwelera m’chimake posachedwapa.
Mkulu wa bankiyi ku Malawi, a Hugh Riddel, anena izi mu mzinda wa Blantyre potsegulira mwambo opereka kafukufuku wa m’mene chuma chikuyendera mdziko muno, Malawi Economic Monitor (MEM).
A Riddel ati pali zinthu zambiri monga kuteteza chuma, kuunikanso ndondomeko yazipangizo za ulimi zotsika mtengo komanso kubwezeretsa chuma m’chimake, zimene zikuonetsa kuti zinthu zinthu zikhala bwino.
Koma iwo apemphanso boma kuti liwonetsetse kuti ngongole zomwe dziko lino lilinazo zikutsika komanso kusiyana kwa ndalama zomwe dziko lino limagwiritsa ntchito pogula katundu kunja komanso zomwe limapeza likagulitsa katundu (trade balance) kudzichepa.
Pa mwambowu palinso nduna yowona za madzi ndi ukhondo, mayi Abida Mia.