Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA yati anthu m’dziko muno akhale tcheru komanso atsatire malangizo malinga ndi malipoti okhudza namondwe Chido amene akuyenda m’nyanja ya mchere (Indian Ocean).
Ofalitsa nkhani ku DoDMA, a Chipiliro Khamula, ati nthambi yoona za nyengo yalosera kuti namondweyu wakula mphamvu ndipo akuyembekezeka kuomba pa gombe la Nacala m’dziko la Mozambique Lamulungu likudzali.
Malinga ndi nthambi yoona za nyengoyi, kuwomba kwa namondweyu kutha kudzetsa mvula yochuluka komanso kusefukira kwa madzi m’madera ena a mdziko muno kuyambira Lamulungu kapena Lolemba pa 16 December.
Pa chifukwachi, DoDMA yapemphanso anthu amene amakhala m’malo amene mumasefukira madzi kuti asamukire ku mtunda kuti ateteza miyoyo komanso katundu.