Malawi Broadcasting Corporation
Local News

Mumba wakhazikitsa mfundo zake

Yemwe akupikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress, MCP, Vitumbiko Mumba wakhazikitsa mfundo zake zokopera nthumwi za ku msonkhano waukulu wa chipanichi ndi cholinga choti akamusankhe pa udindowu.

Mumba wakhazikitsa mfundozi pa msonkhano wa atolankhani ku Mzuzu masana a lamulungu.

Mwa zina, Mumba wati adzatenga gawo lowonetsetsa kuti padzakhale kusiyana pa ntchito za chipani ndi ntchito zotumukira boma la Malawi.

Iye watinso adzaonetsetsa kuti akutumikira ndi kupereka malangizo oyenera kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera, yemwenso ndi mtsogoleri wachipani cha MCP.

Chipani cha MCP, chili ndi msonkhano waukulu kuyambira pa 8 mpaka pa 10 mwezi wa mawa, komwe mwazina, chikasankha atsogoleri a komiti yaikulu yoyendetsa chipanichi.

 

Walemba: Musase Cheyo

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Adopt digital financial services — Reserve Bank

MBC Online

Malawi nears completion of environment report after 15-year gap

McDonald Chiwayula

Wasilikali wachali kupenja ndege iyo wakakwera wachiwiri kwa mrongozi wa charo chino

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.