Chinthuzi: tsamba la Mtukula Pakhomo
Anthu okhala mu mzinda wa Blantyre, amene boma linawayika pa mndandanda wa mtukula pakhomo wammizinda, lero alandira ndalama zawo zokwana K150,000 aliyense.
Kunali kuvina komanso kusekelera ku Ndirande komwe mtolankhani wathu Kumbukani Phiri anaona anthuwa, pomwe nthawi inakwana 2 koloko masana, atayamba kulandira uthenga mufoni zawo kuti mwalowa ndalamazi.
Anthu okwana 43,335 ndiwo alandira ndalamazi zokwana pafupifupi K7 billion ku Blantyre kuti ziwathandize polimbana ndi umphawi.
Boma, kudzera kuthandizo la World Bank kuchokera muthumba lomwe akulithandiza ndi maiko a Iceland, Norway, USAID, EU, UK komanso Ireland, lidati ndalama pafupifupi K16 billion ndizo zithandize anthu a mmizinda yonse inayi yamdziko muno.