Apolisi m’boma la Mangochi amanga a Smith White, 32, powaganizira kuti anaba zipangizo zomangira nyumba za K30 million ku Savijan Cottage komwe amagwirako ntchito ngati mlonda.
Ofalitsa nkhani ku Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daud, ati atachita kafukufuku anapeza kuti a White anagulitsa katunduyi yemwe amangokhala.
A Daudi ati mwini wakeyo atazindikira izi, anakanena ku polisi ndipo apolisiwo anapeza wina mwa katunduyi yemwe ndi wa ndalama zokwana K20 million.