Mpingo wa Manja Seventh Day Adventist mu nzinda wa Blantyre lero ukumalizitsa msonkhano wake wa pachaka wa Misasa omwe unayamba pa 27 August 2024.
Mutu wa msonkhanowu ndi ‘Kusandulika mu chikhalidwe pomwe tikukatumikira’.
Mlaliki wa mkulu pa msonkhanowu ndi mtsogoleri wakale wa Seventh Day Adventist m’dziko muno, abusa Frackson Kuyama.
Mu ulaliki wawo iwo anayamba ndi kulangiza akhristu kuti adzikhala ololerana posasungirana mangawa, kukhala okhutira ndi zomwe ali nazo komanso kusamalira chakudya.