Mwambo wa chionetsero cha ntchito zokopa alendo komanso chikhalidwe wayamba ndi ulendo wa ndawala kuchokera pa Memorial Tower mpakana mu msewu wa Presidential Drive munzinda wa Lilongwe.
Mwambowu, umene wakonzedwa ndi bungwe la Malawi Tourism Council, cholinga chake ndi kulimbikitsa ntchito zokopa alendo ndi chikhalidwe m’dziko muno.
Mfumu ya mnzinda wa Lilongwe, a Esther Sagawa, komanso akuluakulu ena ochita malonda okopa alendo ndi oyimba osiyanasiyana monga Lulu ali nawo pa mwambowu.