Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Msonkhano waukulu wa CCAP Livingstonia Synod wayambika

Akuluakulu a mpingo wa CCAP mu synod ya Livingstonia akukumana ku Embangweni ku tchalichi cha Laudon m’boma la Mzimba.

Moderator wa Mpingowu M’busa Rueben Msowoya akuyembekezeka kutula pansi udindowu ndipo mmalo mwake M’busa Jairos Kamisa ndi amene atenge udindo wa Moderator watsopano.

Nthumwi zikuyenera kuchita chisankho chosankha moderator amene adzatenge udindowo mchaka cha 2026.

Pamapeto pa mkumanowu moderator mogwirizana ndi komiti yayikulu akuyembekezeka  lkusankha adindo atsopano amene agwire ntchito m’mipingo, nthambi ndi mabungwe onse a synodiyi kwa zaka ziwiri zikubwerazi.

Pamwambowu pafika akukuakulu a boma kuphatikizapo Sipikala wanyumba yamalamuro a Catherine Gotani Hara, nduna yaza ulimi a Sam Kawalex ndi alendo ena osiyanasiyana.

 

Olemba  Hassan Phiri

Related posts

A Mnjale amwalira

Mayeso Chikhadzula

CHAKWERA LEADS HUMAN RIGHTS COMMEMORATIONS

MBC Online

NYCOM worried by low youths’ representation in decision-making platforms

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.