Apolisi kwa Chimwala ku Mangochi akusunga mchitokosi Isaac Mathipa wazaka 35 yemwe ndi mphunzitsi wapasukulu ya sekondale ya Chiunda Community Day pomuganizira kuti wagwilira ophunzira wa zaka 15 yemwe ali mu folomu 1 pasukuluyi.
Ofalitsankhani za Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, atsimikiza.
“Malipoti omwe tilinawo ndi akuti pa 30 September 2024, mphunzitsiyu adakumana ndi mtsikanayu akuyenda kuchokera kwa mzake ndipo mphunzitsiyo anamukweza njinga yake yamoto atamuuza kuti akamusiya kwawo, koma mapeto ake mphunzitsiyo analunjika njingayo kunyumba kakwe komwe anakamugwililira,” atero a Daudi.
Mathipa akaonekera kubwalo lamilandu kukayankha mulandu ogonana ndi mwana.