Anthu okhala m’mudzi mwa Kanyenda, dera la mfumu Kabudula chakumpoto kwa boma la Lilongwe tsopano ali ndi madzi aukhondo kutsatira mjigo omwe bungwe la National Water Resources Authority (NWRA) lapereka.
Mfumu Kanyenda yayamika bungweli kaamba ka mjigowo, omwe ndioyamba mmudzimo.
Iwo ati m’mbuyomu, anthu mderali akhala akumwa madzi amumtsinje wa Lingadzi, zomwe zimabweretsa matenda otsekula mmimba.
Phungu waderali, Monica Chayang’anamuno, yemwenso ndi nduna yoona zamigodi, ndi amene anathandizira kuti anthu ake alandire mjigowo ndipo wati naye ndiokondwa ndichitukuko chomwe chabwera mdera lake.
Wapampando wa bungwe la NWRA, a James Mambulu, ati anaganiza zopereka mjigowo ngati njira yothokoza chifukwa anthu mderalo akupitiliza kusamalira mitengo 1800 pa 2000 yomwe anabzala chaka chatha.