Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ndege imene anakwera a Chilima yasowa

Asilikali ankhondo, mothandizana ndi nthambi zina zaboma, ali mkati mofufuza kuti apeze kumene kuli ndege imene inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Saulos Chilima.

Malinga ndi kalata imene wasayinira ndi mlembi wamkulu mu ofesi ya prezidenti ndi nduna zake, a Colleen Zamba, ndegeyo, imene ndiya MDF, imayembekezeka kutera mma 10:02 kummwawa munzinda wa Mzuzu kuchokera ku Lilongwe koma akuti inasowa pa makina amene amaonerapo ndege ndipo siidaonekenso.

A Zamba ati potsatira izi, mkulu wa asilikali ankhondo m’dziko muno, a Valentino Phiri adziwitsa mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera, amene wayimika ulendo wake umene amayenera kunyamuka lero kupita ku Bahamas.

Mtsogoleri wadziko linoyu ndiye walamulanso asilikali ndi ena kuti ayambe kusakasaka ndegeyo.

Malipoti akusonyeza kuti a Chilima amayembekezeka kukakhala nawo pamwambo oyika m’manda a Raphael Kasambara,umene wachitika m’boma Nkhata Bay.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mamembala a COMSIP alimbikitsa ukhondo m’misika

Doreen Sonani

President Chakwera arrives in Mulanje

MBC Online

MIA LAUNCHES K10 MN FOOTBALL TROPHY

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.