Mfumu yaikulu Nkhulambe ya m’boma la Phalombe yamwalira usiku wapitawu.
Malinga ndi bwanamkubwa wa boma la Phalombe, a Douglas Moffat, Mfumu yaikulu Nkhulambe yamwalira itadwala kwa nthawi yochepa.
Pamenepa iwo ati ofesi yawo ndi akubanja akakambirana kuti akonze za tsiku limene ayike mmanda malemu mfumu yaikulu Nkhulambe.