Mfumu yaikulu Mkukula ya m’boma la Dowa yayamika boma chifukwa chowapatsa anthu akwa Mkukula chitukuko cha madzi a m’mipopi.
Mfumuyi yati m’mbuyomu anthu mderali amavutikira madzi koma panopa zinthu zili bwino ndiponso matenda achepa m’derali.
Mfumu Mkukula yatinso ngongole zomwe boma likupereka kudzera ku bungwe la NEEF zikuthandiza anthu ambiri maka amayi ndi achinyamata kuyambitsa bizinesi ndikukhala odzidalira pachuma.
Naye phungu wadera la kummwera chakumvuma m’boma la Dowa, Halima Daudi, wayamika boma chifukwa cha ntchito zachitukuko zosiyanasiyana ndipo apempha kuti lionjezere chiwerengero cha anthu olandira thandizo la chimanga.
Iwo atinso anthu ayambapo kugula feteleza otsika mtengo.