Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

MEC ikuunika zotsatira za chisankho

Bungwe loyendetsa chisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lero likuchita msonkhano ounika momwe zisankho zapadera za pa 23 July, 2024 zinayendera.

Pa msonkhanowo pali mabungwe ndi oimira zipani zandale, mwa ena.

Wapampando wa MEC, Justice Annabel Mtalimanja, wati bungweli linaona kofunika kutero ngati njira imodzi yokonzekera chisankho chimene chichitike chaka cha mawa.

Mwazina, iwo apeza kuti pakufunika mabungwe athandizirepo kumema amayi kuti adzapikisane nawo pa zisankho zikudzazi komanso anthu azindikire zakufunika kolembetsa mukaundula.

Justice Mtalimanja auzanso atolankhani kuti bungweli silichitanso zisankho zina zapadera kuti opikisana akonzekere chisankho cha 2025.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Kodi ndi Arsenal kapena Manchester City?

Emmanuel Chikonso

Mafumu asayina mgwirizano wa chitukuko ndi kampani ya Globe Metals and Mining

Chimwemwe Milulu

Thandizani mpira wa m’maboma — CRFA

Paul Mlowoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.