Bwalo la milandu la Magistrate munzinda wa Lilongwe likuyembekezeka kupereka chigamulo pa pempho la belo la a Chiyanjano Mbedza, amene akuwaganizira kuti amafalitsa nkhani zabodza patsamba la mchezo limene amalitcha Bakili Muluzi TV.
Loya wawo, Gilbert Khonyongwa, ndiye anapereka pempholi lachitatu sabata ino.
Mulanduwu umayembekezeka kuyamba nthawi ya 9 koloko mmawa uno koma wachedwerapo kaamba koti akudikira oweruza.
Mbedza anamangidwa pa 22 July chaka chino mu mzinda wa Blantyre.
Olemba ndi ojambula: Emmanuel Chikonso ndi Thokozani Jumpha