Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi akuchita nawo mapemphero pa mpingo wa Zambezi Evangelical ku Mitsidi mu mzinda wa Blantyre.
Pampingopa palinso chikondwerero chokhazikitsa mlembi wamkulu pa mpingowu, m’busa Robert Yanduya.
Dr Usi analandiridwa ndi abusa komanso akuluakulu ampingowu.