Bungwe loona zachisankho la MEC lalimbikitsa mafumu amdera la mfumu yaikulu Machinjiri Ku Blantyre kuti agwire ntchito ndi mbali zonse mosakondera kuti chisankho chapadera cha khansala, chomwe chichitike pa 23 July chaka chino, chidzayende bwino.
Mmodzi mwa makomishonala a bungweli, a Emmanuel Fabiano, anena izi pamsokhano wa mafumu ku South Lunzu, omwe cholinga chake ndi kuwadziwitsa zambiri zokhudza chisankhochi.
Malinga ndi a Fabiano, kulembetsa maina mkaundula kwa omwe sanalembetse kuchitika kuyambira pa 10 mpaka pa 16 mwezi uno.
Iwo alimbikitsanso anthu kudzatsimikiza, pa 23 ndi pa 24 mwezi uno, ngati maina awo
ali mkaundula.
Kuwodi ya Chilaweni kuchitika chisankho chapaderachi potsatira imfa ya khansala Carol Mdala, yemwe anamwalira pa 22 March chaka chino.