Munthu wina, yemwe akumuganizira kuti ndi mmodzi mwa anthu omwe anaba mfuti komanso teargas pa polisi yaku Nyungwe ku Chiradzulu mwezi watha, wafa apolisi atamuombera pomwe amafuna kuthawa ku Blantyre.
Mneneri wa apolisi m’dziko muno, a Peter Kalaya, ati munthuyu, Mike Banda, anamupeza ali ndi mfuti yomwe anabayo pachipikisheni chagalimoto chimene apolisi anachita pa msewu opita ku Chikwawa, ndipo anaulula kuti zida zina za polisi zomwe anabazo anazibisa pozikwilira pansi mmudzi wina kwa Kapeni m’boma lomweli.
A Kalaya ati Banda anawatengera apolisi mmudzi wina komwe anafukula zidazo, kenaka anayamba kuthawa, zomwe zinachititsa apolisi kuti awombe mfuti.
Panthawi yomwe Banda anakaba zidazo kupolisi yaku Nyungwe, anavulaza mkulu wa a polisi pa malopo pomukhapa modetsa nkhawa, pafupifupi kumupha.