Apolisi ku Nkhunga m’boma la Nkhotakota amanga amuna awiri powaganizira kuti amatsatsa malonda a mwana wazaka zitatu.
Mneneri wapolisi ya Nkhunga, Andrew Kamanga, wati amunawo ndi Pilirani Thumba wazaka 38 yemwe ndi bambo wamwanayo komanso Yohane Watch wazaka 48.
A Kamanga ati apolisiwo anatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti pali abambo ena omwe akugona pamalo ogona alendo pasitolo za pa Dwangwa ndipo akugulitsa mwana.
Apolisiwo atafika pamalopo, anapeza amunawo ndipo atawafunsa anavomera kuti akugulitsa mwanayo.