Komiti ya nyumba ya malamulo yoona zaumoyo yati zipitala zambiri zikulephera kupereka chakudya mokwanira kwa odwala chifukwa cha kuchepekedwa kumbali ya ndalama.
Wapampando wa komitiyi, a Matthews Ngwale, ananena izi m’nyumbayi pamene amapereka lipoti lokhudza kaperekedwe ka chakudya kwa odwala m’zipatala za m’dziko muno.
A Ngwale anati aphungu a komiti yawo anayendera zipatala za maboma a Thyolo, Balaka, Dowa, Rumphi komanso Ntcheu pamene amafuna kukaona m’mene nkhani yopereka chakudya kwa odwala ikuyendera.
Chipatala cha Mzimba chokha akuti ndi chimene chikukwanitsa kupereka chakudya katatu patsiku.
Komitiyi yapempha boma kuti lidzipereka ndalama zokwanira komanso mu nthawi yake kuti mavutowa achepe.