Alimi ambiri a fodya akupitilira kusangalala ndi mitengo yabwino yomwe kampani zogula fodya zikupereka kwa alimiwa kumisika.
Malinga ndi a Musaiwale Kavina, amene ndi mmodzi mwa alimi ku msika wa Kanengo, zomwe zachitika chaka chino ndi zachilendo.
“Tiyamike boma chifukwa cha zomwe lachita, taganizani panopa tikumatha kukambilana ndi wogula fodya pa mitengo zomwe kale kunalibe,” iwo anatero.
Wina mwa fodya yemwe MBC yaona akumugula pa mitengo ya $3.25 mpaka $4.40.
Pamenepa amkatsekulira msika wa fodya wa chaka chino m’boma la Kasungu, Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, adanenetsa kuti akufuna alimi afodya adzidyelera thukuta lawo.
Ku msika wa chaka chino, pali chiyembekezo choti alimi agulitsa makilogalamu 140 million, kuchoka pa 120 million kilogalamu chaka chatha cha 2023.