Bungwe la Malawi Blood Transfusion (MBTS) lati silikutolela magazi okwanira, ofalitsa nkhani ku bungweli m’chigawo cha pakati, a Upile Kaimvi, atero.
Iwo amayankhula izi munzinda wa Lilongwe pamene mpingo wa Lilongwe CCAP Livingstonia Synod unasonkhanitsa achinyamata kuti apereke magazi ku bungweli.
“Ndipofunika kuti aliyense atengepo gawo popereka magazi. Tiyamike zomwe wapanga mpingowu, moyo wina wake upulumuka ndithu,” a Kaimvi anatero.
M’mawu ake, m’busa wa mpingo wa Lilongwe CCAP, a Nase Chunga, anati ndi udindo wa anthu opemphera kupereka magazi chifukwa kusowa kwa magazi muzipatala ndi vuto lalikulu limene boma palokha silingakwanitse kuthana nalo koma aliyense atengepo gawo.
M’modzi wa achinyamata amene anapereka nawo magazi, Cynthia Chipenda, anatsutsa zakuti munthu akapereka magazi amadwala
Iye anati aka kanali kachitatu iye kupereka magazi koma sanadwale.