Bungwe la Independent Schools Association of Malawi (ISAMA) lati lipitiriza kugwira ntchito ndi mamembala ake polimbikitsa maphunziro a atsikana m’dziko muno.
Mkulu wa bungweli, a Bishop Wycliffe Chimwendo, ndi amene ananena izi pamene sukulu ya Vakusi Model High ya m’boma la Ntcheu imapereka mphoto ya ulendo wapandege ochoka ku Chileka kupita ku Lilongwe kwa ophunzira yemwe anakhoza bwino pasukuluyi m’mayeso a Form 4 apitawa, Victoria Lunduka, amene anakhoza 12 Points.
Victoria anati chinsinsi chake chakhala kulimbikira kotero walimbikitsa asungwana anzake kuti asamazikaikire.
Mphunzitsi wamkulu wa sukuluyi, a Keston Kapalamula, anati potsindika kuzipereka kwawo pa ntchito za maphunziro, atsikana ochita bwino pasukulu yawo amawapatsa ma scholarship.