Mai wa fuko lino, Madam Monica Chakwera, lero akutsogolera amayi m’dziko muno pa mwambo wa tsiku la mapemphero a amayi pa dziko lonse.
Mwambowu ukuchitikira pabwalo la masewero la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.
Pa 1 March chaka chilichonse ndi tsiku limene linapatulidwa kukhala tsiku la mapemphero a mayi pa dziko lonse.
Mutu wamapempherowa chaka chino ndi “Ndikupemphani inu kulolerana wina ndi mzake mwachikondi” (Aefeso 4:1-8).