Apolisi ku Lilongwe amanga a Ruth Nkhoma powaganizira kuti anapha amuna awo a Misheck Bayison powakoka ndi kupotokola ziwalo zobisika kaamba kakusamvana pa ndalama yokwana K40,000 imene bambowa adamwera mowa.
Malinga ndi ofalitsankhani wa Polisiyi, a Hastings Chigalu, mayiyu ataona kuti mwamuna wake wafa, anakonza ngati kuti adadzipha yekha podzimangilira koma madotolo atapima thupi la malemuwa anatsutsa izi.
A Bayison anali a m’mudzi wa Nyenyezi kwa mfumu yayikulu Malemia m’boma la Nsanje pomwe a Nkhoma amachokera m’mudzi wa Thonyiwa kwa mfumu yayikulu Nsabwe m’boma la Thyolo.