Bwalo lazamasewero la Katoto lero latangwanika chifukwa kukuchitika ndime yotsiriza ya chikho cha Mayor’s cha masewero a Mpira wamiyendo komanso wamanja.
Mwambowo wayamba ndi ulendo wa ndawala kuchoka kuma office a Mzuzu City Council kuyenda mu Highway kukafika pabwalo lazamasewero la Katoto.
Ena mwa amene anali nawo pa ulendowu ndi Mayor wa Mzinda wa Mzuzu a Kondwani Nyasulu, mkulu oyendetsa ntchito za mu mzindawo a Gomezgani Nyasulu, ma Khansala, ndi adindo ena osiyanasiyana kuphatikizapo akukuakulu a bank ya FDH amene akuthandiza chikhochi ndi ndalama zokwana K17 million.
Matimu a primary school a Zolozolo akumana ndi Chibavi mu masewero a mpira wa manja, pamene matimu a Mzuzu CCAP akumana ndi Katoto Primary School mu ndime yotsiliza ya Mpira wamiyendo wa anyamata.
Olemba: Hassan Phiri