Thupi la yemwe anali muulutsi ku MBC, mayi Everess Kayanula, anyamuka nalo mawa kuchoka ku Blantyre kupita kumudzi kwawo kwa Msiro, mfumu yayikulu Kayembe m’boma la Dowa.
Mayi Kayanula, amene anayamba ntchito ku bungwe la MBC pa 16 March 1983 ndipo anapuma ntchito pa 1 August 2018, anamwalira usiku wa lachisanu ndipo akuyembekezeka kulowa mmanda lachiwiri likudzali.
Mchimwene wa malemuwa, John Chintolo, wati asananyamule zovutazi kupita ku Dowa, pakakhala mwambo wamapemphero amene akachitikire ku College of Medicine mu mzinda wa Blantyre.
Pakadali pano, maliro akulilira kunyumba kwa mayi Kayanula ku Area 6 ku Machinjiri mu mzindawu.
Iwo anayamba ntchito ku MBC ngati othandizira muulutsi wa pa wailesi (Assistant Announcer) ndipo anapuma pa ntchito ali Controller of Current Affairs.