Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, lero anyamuka ku Lilongwe kupita mchigawo chakumpoto kumene akayendere ntchito zina zachitukuko.
Malinga ndi kalata imene wasayinira mlembi wamkulu mu ofesi ya President ndi nduna zake, a Colleen Zamba, mwazina Dr Chakwera akakhala nawo pamwambo watsiku lokumbukira anthu amene adadzipereka kuti dziko lino likhale pa ufulu (Martyrs Day).
Mwambowu umakhalapo pa 3 March chaka chilichonse ndipo chaka chino tsikuli likhala pa lamulungu (Sunday).