Thupi la malemu Patricia Shanil Dzimbiri alitengera ku mudzi kwa Mfulanjobvu, kwa Kangamkundi m’dera la mfumu yayikulu Chamthunya m’boma la Balaka komwe akaliyike m’manda.
Kuyambira ku m’mawaku, kunali Misa yolemekeza mzimu wa malemuwa imene imachitikira ku nyumba ya chisoni ya Sunset Funeral Services ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe.
Archbishop Tambala a Archdiocese ya Lilongwe ndi amene amatsogolera mwambo, kumene kunali mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera, mayi wa pfuko Monica Chakwera, komanso atsogoleri akale a dziko lino Dr Bakili Muluzi ndi Dr Joyce Banda pamodzi ndi amuna awo Justice Richard Banda.
Dr Chakwera asanafike pa malo a chisoniwa, nduna yoona maboma a ang’ono a Richard Chimwendo Banda, inati mtsogoleriyu ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfayi kaamba kakuti malemuwa anagwira ntchito yayikulu potumikira dziko lino.
Malemu Patricia Shanil Dzimbiri anabadwa m’chaka cha 1964 pa 25 September ndipo anakhalako mayi wa pfuko zaka za m’mbuyomo, komanso adakhalakonso phungu wa nyumba ya malamulo m’zaka za 2014 mpakana 2019 ku nzambwe kwa boma la Balaka.
Iwo amwalira pamene anachita ngozi ya ndege limodzi ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Klaus Chilima dzana, Lamulungu mu nkharango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.