Mtsogoleri wa dziko lino, Dr.Lazrus Chakwera, akhala nawo pamwambo wa nsembe ya Misa ya mayi Shanil Dzimbiri kunyumba ya chisoni ya Sunrise ku Kanengo munzinda wa Lilongwe.
Mayi Dzimbiri m’mbuyomu anali anali mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bakili Muluzi, ndipo mwambowu ndiwoperekeza thupi lawo kumudzi kwawo ku Balaka komwe akuyembekezeka kukayikidwa mmanda mawa pa 14 June.
Atsogoleri akale adziko lino Dr.Bakili Muluzi komanso Dr.Joyce Banda ndi Retired Chief Justice Richard Banda afika kale, kuphatikizapo ana amalemu Shanil ndi nduna zambiri zaboma ndi akuluakulu ena.
By Mirriam Kaliza