Timu ya Silver Strikers yalemba ntchito Peter Mponda ngati mphunzitsi wa timuyi amene akulowa m’malo mwa Pieter De Jongh yemwe adatula pansi udindo wake mwezi wathawu.
A Mponda awapatsa kontarakiti ya chaka chimodzi komanso awapatsa ufulu osankha mphunzitsi owathandiza.
Mkulu oyendetsa ntchito ku timuyi, a Patrick Chimimba, ndi amene atsimikiza za nkhaniyi pomwe amalandila mphunzitsiyu pa bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe Lamulungu masana.
Poyankhulapo, a Mponda anapempha otsatira timuyi kuti akhulupilire ntchito imene agwire posatengera za mbiri yakale.
Mphunzitsi-yu, watsogolerako ma timu monga Premier Bet Wizards, analinso wa chiwiri kwa mphunzitsi wa timu ya Bullets, komanso chaposachedwapa anali akuphunzitsa timu ya Black Leopards ya m’dziko la South Africa.
Olemba: Foster Maulidi.
#mbconlineservices