Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Mpingo wa Katolika wataya mkhristu wokhulupirika

Pamene mwambo wokhuza maliro a wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, malemu Dr Saulos Chilima, ukupitilira ku Area 12, mtsogoleri wa bungwe la Mayi Maria mu mpingo wa Katolika mu dayosizi ya Lilongwe ndi ma dayosizi ena mdziko muno, Dr Mary Shawa, wati parishi ya St. Patrick’s komwe malemu Chilima amapemphera komanso dziko la Malawi lataya mtsogoleri yemwe anali ndi masompheya.

Dr Shawa, omwenso adapuma ngati ndi mlembi wamkulu m’boma, ati adzawakumbukira Dr Chilima ngati mkhristu wodzipereka ku ntchito ya Mulungu komanso ku dziko.

Lero ndi tsiku lachinayi dziko lino likukhuza malirowa kuchokera pomwe thupi la a Chilima ndi ena asanu ndi atatu anafa pa ngozi ya ndege.

Thupi la a Chilima likuyembekezeka kulowa m’manda lolemba sabata ya mawa kumudzi kwawo ku Ntcheu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Namondwe Filipo alibe chiopsezo ku Malawi, atero azanyengo

Romeo Umali

Sitima yapakati pa LL, BT iyambanso kuyenda — Hara

MBC Online

Ogonana okhaokha chigamulo mawa

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.