Unduna wa za maboma ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe wapempha akubanja kwa malemu mfumu Mgulumia ku Machinga kuti atsate ndondomeko zonse zoyenera posankha mfumu ina yatsopano.
Mlembi wamkulu mu undunawu, Elizabeth Gomani Chindebvu alankhula izi pa mwambo oika mmanda thupi la malemu Mgulumia ku Likwenu ku likulu la mfumuyi.
“Nthawi ikafika yosankha mfumu yatsopano, kambilanani mwabata motsata chikhalidwe cha kuno komanso malamulo aboma kuti pasakhale ziwawa,” watero mlembiyu.
Malinga ndi mlembiyu, nthawi zambiri kusamvana pa za mlowammalo wa mfumu kumabwenzeletsa m’mbuyo ntchito za mmadera pamene mfumu ya mwalira.
Mmau ake mfumu yaikulu Chamba yomwe inaimila mafumu a Ndodo m’bomali yati malemu mgulumia anali mfumu odzipereka polimbikitsa umodzi komanso ntchito za chitukuko.
Mfumu Mgulumia omwe dzina lawo lenileni ndi a Magret Askimu Mlomba amwalira dzuro loweruka ku Machinga atadwala kwa kanthawi.
A Mgulumia omwe anabadwa pa 12 october mchaka cha 1971 asiya ana anayi ndi zidzukulu ziwiri.
Olemba: Owen Mavula