Nduna yoona zachitetezo m’dziko la Zambia, a Ambrose Lwiji Lufuma, yati dziko lawo lili ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya wachiwiri kwa mtsogoleli wa dziko lino, Dr Saulos Chilima.
A Lufuma atsogolera nthumwi za dzikolo, ndipo ati Prezidenti Hakainde Hichilema atamva za ngozi adaonetsetsa kuti athandize mtsogoleri nzawo kuno pa ngoziyi.
“Ubale wamaiko awiriwa ndi wakale kwambiri kotero kuti chilichonse chomwe chagwera dziko la Malawi, chagweranso dziko lathu la Zambia,” anatero a Lufuma.
Wachiwiri woyamba kwa sipikala wa nyumba ya malamulo ya dziko lino, a Madalitso Kazombo, ati zomwe lachita dziko la Zambia ndi chitsimikizo cha ubale wabwino omwe ulipo pakati pa maiko awiriwa.
Iwo anati dziko la Malawi lataya munthu wofunikira osati kuno kokha komanso mdera lonse la Africa.
Zina mwa nthumwi zomwe zachokera m’dziko la Zambia nkuphatikizapo mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma m’dzikolo.