Yemwe adaali m’modzi wa akuluakulu kuchipani cha Democratic Progressive m’chigawo chakumpoto ndipo adalowa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Joe Thomas Nyirongo, wati ndikulakwa kumafalitsa kanema yemwe cholinga chake ndikufuna kusokoneza anthu m’dziko muno.
Iwo ati pamene aMalawi akukhuza maliro a wachiwiri kwa mtsogoleli wadziko lino, malemu Dr. Saulos Chilima, pakufunika chikondi komanso kulolerana m’malo momafalitsa zinthu za bodza monga ena akuchitira.
Malinga ndi chikalata chomwe a Nyirongo atulutsa, iwo atsutsa kuti kanemayo ndi watsopano.
“MCP itapambana madera onse amakhansala [m’boma la Karonga] ndidali wokondwa kuti zinthu zilibwino ndi momwe chayandera chisankho osati zomwe ena akuchita pofuna kunamiza a Malawi, ” iwo anatero.
Iwo ati ndizokhumudwitsa kuona kuti anthu ena amaganizo oyipa wosakonda dziko la Malawi akufalitsa mbali Ina ya kanemayo pongofuna kusokoneza anthu mdziko muno.
Iwo ati chipani cha DPP chilibe mphamvu m’chigawo chakumpoto ndipo chidatha chikoka, zomwe zachititsa kuti adzifalitsa zabodza.
Iwo ati aMalawi ndi anthu woopa ndikukonda Mulungu, kotero kuti apewe kumvera zomwe anthu ena amaganizo woipa adzifalitsa pomwe dziko lino lili pa chisoni chifukwa chotaya Malemu Dr Chilima.