Akubanja la Malemu Dr Saulos Chilima ati ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfa ya m’bale wawo yemwe anali mzati wa banjali.
M’mau awo, a Ben Chilima omwe ndi mchimwene wa malemuwa, anayamika onse omwe anatengapo gawo pofufuza ndege yomwe idali itasowa mu nkhalango ya Chikangawa.
Iwo anayamika boma chifukwa chathandizo losiyanasiyana lomwe lapereka pa chipsyinjochi.
Iwo anati akubanja anali wokondwa kuona kuti anali ndi mwayi okhala nawo panthawi yomwe amapima thupi la malemu Dr Chilima.
Mwa zina, iwo anati akadakondabe kuti pakhale kafukufuku okwanira kuti adziwe chomwe chidachititsa ngozi ya ndege pofuna kupewa ngozi za mtunduwu mtsogolo muno.
Iwo ati ndi wokondwa kuti zinthu zonse za malemu Dr. Chilima zomwe zidasowa pamalo angozi tsopano zili ndi akubanja.
A Ben Chilima ati Dr. Chilima anali mphunzitsi kwa anthu ambiri omwe anati anasintha miyoyo yawo ndipo amakonza zofuna kusintha mudzi wakwawo.
Iwo alimbikitsa anthu onse mdziko muno kuti asayipitse mbili ya malemu a Chilima, omwe anati anali okonda umodzi ndi mtendere.