Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Malawi Fertilizer Company itha kupanga fertilizer okwana 150, 000 tons

Mkulu wa fakitole ya Malawi Fertilizer Company, a Christopher Keen, ati ili ndi kuthekera kopanga ma tani okwana 150, 000 a feteleza pa chaka.

A Keen amayankhula kwa alimi oposa 100 a minda ikuluikulu amene amayendera kampaniyi ku Liwonde kuti apeze mwayi odziwa m’mene feteleza amagwirira ntchito mu nthaka komanso kudziwa feteleza oyenera pamunda wawo kuti akolole zochuluka.

M’modzi mwa alimiwa, a Jonathan Kamakanda, anati chiyambire ntchito ya minda ikuluikulu, iwo akupeza phindu.

Iwo anati izi zili chomwechi chifukwa boma layika njira zabwino zobweretsera pamodzi akatswiri pa zaulimi m’magawo ambiri amene akuwathandiza kudziwa bwino za feteleza ndi nthaka.

Oyang’anira ntchito ya minda ikuluikulu ku unduna wa zaulimi, a MacDonald Chikhawo, anati ntchito yawo ndi alimi ena ikuonetsa tsogolo labwino kaamba koti nthambi zonse zokhudzidwa ndi ulimi zikuonetsa chidwi chothandiza alimi kutukuka monga mwa masomphenya a Malawi a 2063.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Titangwanike pomanga dziko lino – Chakwera

Beatrice Mwape

Amumanga ataba mu kachisi

Charles Pensulo

Ntchito yojambula msewu wa Makanjira-Mangochi igwiridwa mwachangu

Eunice Ndhlovu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.